Sitikufuna kubweleranso kwathu-atero mayi Hanoki

Advertisement

Mai Bertha Hanoki, ochokera m’boma la Nkhotakota amene akukhala pa msasa wa Ngala ngati malo omwe akukhala anthu omwe anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi, ati iwo sakufunanso kubwerera ku mudzi kwawo ku Kanthum’dende komwe anaona mavuto kamba ka kusefukira kwa madzi.

Poyankhura ndi nyumba yolemba Nkhani ino, mayi Hanoki ati mudzi wa Kanthum’dende, mfumu yaikulu Kanyenda ndi mudzi omwe unakhuzidwa kwambiri ndi madzi ndipo zinthu ngati zifuyo ,ziwiya zapakhomo , nyumba ndi zina zambiri zinakokoloka nkusiya anthu ali kakasi.

Mayiyu wati sali okonzeka kubweleranso kwawo potengera kuti anthu ena omwe ndi achibale anatsikira kuli chete kamba ka ngoziyi ndipo iwo awona kuti nkwabwino kuti a boma awathandidze kupeza malo abwino okhala n’cholinga choti atetezedwe.

“A boma chonde tikupempha kuti mutithandize kupeza malo abwino. Moyo wakuno ku ndi ovuta, kudya nkovutikira ,kugona kumene nkovutanso potengera kuti tilipo ochuluka. Ndikunena pano ana, athu anasiya kupita ku sukulu kalekale chifukwa chilichonse chinasonekera,” atero mayi Hanoki.

Mayiyu yemwe ndi wa zaka 34 zakubadwa ndipo ali ndi ana asanu ndi banja, ati  angakondwe atakhala ndi ndalama yoyambira bizimesi n’cholinga choti adzikwanitsa kupeza chakudya potengera kuti ma bungwe komanso ena othandiza amatha kutenga nthawi yaitali asanabwere kudzagawa zakudya zomwe zimapangitsa kuti azigwira maganyu kuti apeze chakudyachi.

Milanzi akupempha thandizo

Poyankhurapo, Madalitso Milanzi yemwe ndi nyamata wa zaka 24,  wati khumbo lake ndilofunanso kuyambiranso sukulu potengera kuti waona anthu ambiri akuchita bwino chifukwa chophunzira ndipo akupempha anthu akufuna kwabwino kuti amuthandize ndi zipangizo monga makope ndi zina.

Oyimira ku m’thambi yowona zangozi zogwa mwadzidzidzi m’bomali a John Manda ati akuyesetsa kuti anthu amene akukhala ku misasayi akhale moyo wabwino komanso akufuna kuti pobwelera m’madera omwe amakhala, akhale ndi zoyenereza zokayambira moyo wina watsopano.

Pa msasa ya Ngala pali anthu anthu okwana 337. Abambo alipo 144, amayi alipo 222 ndipo ana alipo 44. Amayi oyembekezera alipo 25 ndipo awulumari alipo 25.

Pa msansawu palinso misasa ina iwiri yomwe ndi Matiki yomwe ili ndi anthu 339. Abambo alipo 130, amayi alipo 130, awulumari alipo 3. Msasa wa Nyamvu ndi omwe uli waukulu ndipo uli ndi anthu 1158. Mwa anthu amenewo, 460 ndi abambo, 220 ndi amayi ndipo 290 ndi ana, awulumari alipo asanu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.