Ndi okuba mzathu Chilima – watelo Dausi

Advertisement
Dausi

Chipasupasu chija chafika. Wina kwake, winanso uko. Wadya balalikani akuchitika ku chipani cholamula cha DPP.

Mneneri wa boma a Nicholas Dausi adzudzula kolimba wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima kamba konena kuti mu boma muli kuba ndi katangale zoopsa.

Nicholas Dausi
Dausi: Ndi okuba mzathu Chilima

A Chilima adanena pa mwambo wa mpingo wa katolika ku Ntchisi kuti mu boma la DPP muli katangale oopsa amene angapangitse kuti iwo achoke mu chipani.

Koma poyankhapo pa Nkhaniyi, a Dausi anati a Chilima sakuyenela kupita ku gulu ndikukanyoza utsogoleri umene wachiwiri wake ndi iwo omwe.

“A Chilima ndi wachiwiri mu utsogoleri akunenawu ndipo iwo amayenela kupeleka uphungu osati kunyoza iyayi,” anatelo a Dausi.

A Dausi anati ngati mbiri ya boma ili ingakhale ya katangale, sikuti a Chilima angapatuke iyayi.

Pa nkhani yoti a Chilima adanenapo kuti pamene katangale wafika mu boma la DPP ndizopangitsa bandi kugawana zida, a Dausi anati angathe kuyankhula pa zimenezo ndi a Chilima eni ake.

“Amene ananena zimenezo ndi a Chilima, aloleni iwo eni amasulire zimene amatanthauza,” anatelo a Dausi.

Advertisement

One Comment

  1. CHILIMA APANGE CHIPANI CHAKE LIMODZI NDI KALI/SITA/ATI/NDO NDI EMAWO. BBBAAASSSIII…

Comments are closed.