Nyumba ya malamulo mu nzinda wa Lilongwe lachiwiri yadutsitsa ma bilu ya chi 28 ya mchaka cha 2024 ndi bilu ya chi 29 yolola kuti boma lidzitha kugula mafuta a galimoto kudzera mu mgwirizano wa boma ndi boma popanda a mkhalapakati (government to government).
Nduna yowona za mphamvu ndi magetsi, a Ibrahim Matola ndi omwe inabweretsa bilu-yi kutsatira zomwe analengeza mtsogoleri wa dziko masiku ochepa apitawo kuti athe kuthana ndi mavuto akusowa kwa mafuta amene akuta dziko lino mopyola mulingo.
A Matola ati kampani za NOCMA komanso PIL ndi omwe apitilize kubweretsa mafuta m’dziko muno ndipo anawonjezera kuti njirayi ithandiza kuti mitengo ya mafuta ikhale yosaphinja aMalawi.
Isanadutsitse Bilu-yi amene analankhulira chipani cha DPP , a Bright Msaka anati nduna ya zamagetsi ikumbuke zomwe section 12 ya malamulo a dziko lino amanena zokhudza kuchita zinthu poyera.
A Msaka anati ndunayi ikutenga zonse zokhudza kugula mafuta ndipo kuti sangafunsidwe chifukwa akhala pamwamba pa lamulo.
Iwo anati anthu adzadziwa bwanji kuti mitengo yomwe boma lidzigulila mafuta ikhala yowona? komanso ndondomekoyi idzetsa mavuto kuposa ali pakali pano.
A Msaka anati cholinga cha bilu ya chi 29 yomwe ikufuna kubweretsa ndondomeko ya boma ndi boma ndi kufuna kudzasiya ngongole zambirimbiri akamadzachoka m’boma ndipo ati njirayi ndi yobela ndalama za boma komanso kusonyeza kukanika kuyendetsa zinthu ndi kusowa nzeru pa m’mene angathanilane ndi mavuto.
Oyankhulira UDF yemwenso ndi phungu wa dela la Machinga east, a Esther Jolobala ati bill yi ikudza chifukwa kulibe ndalama zaboma ndipo zipha NOCMA, MERA , PPDA ndi kupitsa mphamvu ku boma kokha.