Aloleni anthu azigwilira ntchito ku nyumba mafuta avuta, AFORD yawuza boma

Advertisement
Fuel Crisis

Potsatira vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto, chipani cha Alliance For Democracy (AFORD), chapempha boma kuti liwuze anthu ogwira ntchito m’boma kuti kwa pano pokha azigwilira ntchito ku nyumba monga zinaliri nthawi ya mliri wa Covid-19.

Izi zili mu kalata yomwe chipanichi chinatulutsa posachedwapa pogwilizana ndi ganizo lochita ziwonetsero zomwe lakoza bungwe la CDEDI zomwe zimayenera kuchitika Lachinayi koma zalepheleka.

Kudzera mu kalatayi yomwe anasayinira ndi wofalitsa nkhani wake, Annie Amatullah Maluwa, chipani cha AFORD chati izi zitha kuthandiza kuchepetsa kupsinjika pa nkhani ya mayendedwe komwe ogwira ntchitowa akukumana nako kaamba kakusowa kwa mafutawa.

“Vuto lomwe liripoli likufuna kuchitapo kanthu mwachangu, ndipo tikulimbikitsa boma kuti liwuze onse ogwira ntchito m’boma kuti azigwira ntchito kunyumba monga momwe zidakwaniritsidwira pa mliri wa Covid 19,” yatelo AFORD. “Izi zithandizira kuchepetsa chipsinjo chakudza kaamba kakusowa kwa mafutawa pachuma komanso moyo watsiku ndi tsiku wa anthu.”

Mu kalata yomweyi, AFORD inalengeza kuti idzatenga nawo gawo pa ziwonetsero zomwe yayitanitsa CDEDI zomwe tsopano zichitika Lolemba pa 25 November 2024. Chipanichi cha me ma otsatira ake kuti adzatuluke mwaunyinji pa tsikuli.  

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.