Mabungwe apanga mgwirizano ofuna kusaka ndalama

Advertisement
Gymkhana Club ground

Mgwirizano wa mabungwe omwe si aboma m’boma la Zomba udzakhala ndi zochitika Loweruka lino pa bwalo la Gymkhana pofuna kupeza ndalama zogwilira ntchito zachifundo monga kukonzanso malo osungira anthu oganiziridwa kuti apalamula milandu ya upandu ku polisi ya Zomba komanso kuthandizira ophunzira ovutika a sukulu za sekondale.

Mmodzi mwa akulu akulu omwe akukonza zochitikazi, Wilkens Nakanga, wati mabungwewa akufuna kupeza ndalama zokwanira 61 Million Kwacha pofuna kuti amangile malo osungila anthu oganiziridwa kuti apalamula milandu ya upandu ku polisi ya Zomba komanso amangire malo odikilira anthu omwe amapita kukawona achibale omwe akusungidwa ku polisi.

Nakanga adati izi zikubwera potsatira pempho lomwe mkulu wa apolisi m’bomali adapempha mabungwewa kuti awathandize.

Iye adati zochitikazi zidzayamba ndimasewero amajowajowa, ulendo wandawala motsogozedwa ndi Police Brace Band komanso zochitika zina monga zokudya, zokumwa, phada, masewero ampira wamiyendo ndi wamanja, zokhwasula khwasula komanso kuvina.

Mabungwewa akufunanso kupeza ndalama zothandizira ophunzira ovutika makumi awiri a msukulu za sekondale omwe akulephera kulipira ndalama za sukulu komanso kupeza zosowa zawo pamaphunziro.

“Tikupempha kuti anthu adzabwere pa bwalo lazamasewero la Gymkana kuti adzatithandize ndikangachepe pofuna kuti zofuna zathu zopeza ndakama zogwilira ntchito zachifundo zikwaniritsidwe,” iwo anatero.

Pakadali pano pano, mmodzi mwa anthu okhala mu mzinda wa Zomba a Anderson Miwanda ati ganizo lomwe achita ma bungwewa ndilabwino kwambiri popeza ophunzira ovutika ambiri akumalephera sukulu chifukwa chosowa thandizo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.