Chakwera asaikire kumbuyo Israel pa nkhondo ya ku Gaza – Abbas


Chakwera asaikire kumbuyo Israel pa nkhondo ya ku Gaza - Abbas- Malawi24

Bungwe la Ulama Council of Malawi lapempha mabungwe omenyera ufulu wachibadwidwe, atsogoleri a ndale, komanso atsogoleri azipembedzo kuti adzudzule zomwe boma la Malawi likuchita pa nkhani yolimbikitsa dziko la Israel kupha mtundu wa Mapalestina.

Polankhula ndi atolankhani mu mzinda wa Blantyre, mlembi wamkulu wa bungweli Sheik Abbas Vinjenje wadzudzula boma la Malawi povota motsutsana ndi kuthetsa nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa Israel ndi Palestine.

Vinjenje waonetsa kukhumudwa ponena kuti dziko la Malawi ndi dziko lokhalo mu Africa muno limene linavota mokomera dziko la Israel kuti lipitilize kuthira nkhondo ku Palestine ndi West Bank pa msonkhano waposachedwapa wa United Nations General Assembly.

“N’zokhumudwitsa kuti dziko la Malawi ndi dziko lokhalo mu Africa lomwe lidavota kuti dziko la lsraeli lipitilize kuthira nkhondo anthu a mtundu wa chi Palesitina,” adatero Vinjenje.

A vinjeje Ananenanso kuti: “Pamsonkhano waukulu wa UN wa chaka chino, mayiko ambiri adavota kuti nkhondo ya pakati pa Israeli ndi Palestina iyime kaye ndipo njira za zokambirana za mtendere zikhazikitsidwe.

Sponsored

LBungweli lalangizanso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti adzudzule mtchitidwe wa uchigawenga omwe dziko la Israel likuchita kwa anthu aku Palestina.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading