Bwalo liyimitsa mulandu wa wapolisi mpaka lachitatu sabata yamawa

Advertisement
Zomba Court

Bwalo lamilandu ku Zomba layimitsa mulandu wa wapolisi wina Sergeant Twaliki Paweni yemwe akumuzenga mulandu chifukwa chomuganizira kuti adagwilira mtsikana wa zaka 14 mwezi wa August chaka chatha.

Paweni akumuganizira kuti adapanga za upanduzi pa nthawi yomwe mtsikanayu adali m’manja mwa apolisi ndipo adamuwuza usiku kuti agone naye kuti amutulutse akhale mfulu.

Mbali ya boma, Lachitatu inabweretsa mboni zisanu zomwe zitatu mwa izo ndi apolisi, modzi wachipatala ndipo mmodzi ndiyemwe adali wapampando woona zachitetezo chakumudzi mdera la Kachulu kunyanja ya Chilwa.

Poyankhula ndi atolankhani, mmodzi mwa yemwe akuyimilira mtsikanayo pa mulanduwo, Vitumbiko Mbizi, wati pakadali pano patsala mboni ziwiri kuti ziperekere umboni wawo.

Mbizi yemwe ndiwochokera ku Bungwe la Women Lawyers Association wati ndiwokhutitsidwa ndi momwe mboni zawo khumi (10) zaperekera umboni wao chiyambire cha mulanduwu ndipo wati zatsala mboni ziwiri kuti zitsilize kupereka umboni wawo popeza mboni zonse zilipo khumi ndi ziwiri. (12)

Koma mmodzi mwa omwe akuyimilira wapolisiyu Alfred Masamba yemwe ndiwochokera ku Bungwe la Legal Aid wati akungodikilira kuti mboni zitsilize kupereka umboni wao.

Yemwe akumva mulanduwu Principal Resident Magistrate Martin Chipofya wayamba wayimitsa mulanduwu mpaka Lachitatu sabata yamawa pa 16 October, 9 koloko mamawa

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.