Kulira komwe kukuganizilidwa kut ndikuwombera kwa mfuti kunamveka pa msonkhano wa a Donald Trump ku dera la Pennsylvania pomwe mtsogoleri wakale wa dziko la America’yu amalankhula.
A Trump anachotsedwq mwa nsanga ndi akuluakulu anthambi ya chitetezo ya “Secret Service”.
Zithunzi zinamuwonetsa iye atakwiya ndikukweza dzanja ku khutu lake lamanja, asanawerame pansi, pemene kulira kwa kwa mfuti kunapitilira kumveka.
Posakhalitsa, asilikali a Secret Service omwe ankamuyang’anira anamuthamangitsa ndipo anamukokera pa siteji n’kupita naye m’galimoto yodikirira.
Malingana ndi zomwe zalembedwa pa tsamba lawo la Truth Social, a Trump ati chipolopolocho chinadutsa “pamwamba” khutu lakumanja. Pomwe pamayambiliro m’neneri wake adati “akupeza bwino” ndipo akulandira chithandizo kuchipatala chakumaloko.
“Ndinaziwa nthawi yomweyo kuti pali chinachake chaupandu chifukwa ndinamva kulira kwa mfuti, ndipo nthawi yomweyo ndinamva chipolopolo chikuphulika pakhungu,” a Trump analemba. “Ndinatuluka magazi kwambiri moti ndinazindikira zimene zimachitika.
Magazi anaonekera kukhutu ndi kumaso kwa a Trump pamene akuluakulu a chitetezo amawachotsa pamalopo.
Munthu yemwe akuganilizidwa kuchita za mtopolazo adawomberedwa pamalopo ndi apolisi a Secret Service, mneneri wa achitetezowa a
Anthony Guglielmi adatelo.
Iwo ananenanso kuti munthu m’modzi adawomberedwa ndipo ena awiri avulala modetsa nkhawa.
Ku America kuli chisankho chosankha mtsogoleri ndipo a Trump, omwe adaluza mpandowu kwa a Joe Biden, apikisananso mu mwezi wa November.