Pomwe panali chiopsezo choti namondwe otchedwa Filipo atha kufika kuno ku Malawi, nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo m’dziko muno yati namondweyu tsopano wabwelera ku nyanja ya nchere ya India komwe anachokera, komabe yati mvula ya mphamvu ipitilirabe kugwa.
Kumayambiliro kwa sabata ino nthambiyi inachenjeza kuti namondwe Filipo yemwe anafika mdziko la Mozambique Lamulungu lapitali, atha kufika m’dziko muno makamaka ma boma a kumwera ndipo panali chiopsezo choti atha kupangitsa mvula kugwa yochuluka zomwe zingapangitse kuti madzi asefukire.
Koma Lachitatu pa 13 March, 2024, nthambiyi yalengeza kuti tsopano namondwe Filipo safikaso mdziko muno kuchokera m’dziko la Mozambique kamba koti watembenuka ndikuyamba kubwelera kulowera ku nyanja ya nchere ya India komwe anachokera.
Nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengoyi, yafotokoza kuti izi zikutanthauza kuti mvula ya mphamvu yomwe madera ena mdziko muno amayembekezera kulandira kamba ka namondweyu, siyifikaso.
“Nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti Namondwe FILIPO akupitiliza kuyenda kulowera m’nyanja ya m’chere ya India kuchokera ku Maputo ku Mozambique lero pa 13 March 2023. Namondweyu apitiliza kuyenda m’nyanjayi kutalikirana ndi malo kokhala anthu, ndipo alibe chiopsezo ku nyengo yaku Malawi,” yatelo nthambi ya za nyengo.
Ngakhale zili choncho, nthambiyi yati kuno ku Malawi mvula yamphamvu ndi yamabingu ipitilirabe kugwa mmadera ena chifukwa cha nkumano wa mphepo yochoka kumpoto chakumvuma ndi kumpoto chakunzambwe, osati chifukwa cha namondweyu.
Choncho nthambiyi yalangiza makolo kuti asalore ana kusewera m’malo akufupi ndi mitsinje, ngalande zodutsa madzi kapena madera osefukira madzi.
Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo yati ipitiriza kauniuni wa nyengo yaku Malawi komanso madera ozungulira ndipo pakakhala nyengo yodzetsa chiopsezo ku dziko lino, nthambiyi yati idziwitsa anthu mdziko muno moyenera.