Boma lapemphedwa kuti liunikenso misonkho ya galimoto

Advertisement

Malingana ndi kukwera kwa misonkho ya galimoto m’dziko lino, bungwe lomwe limayang’anira zokhudza galimoto zowilitsidwapo kale ntchito la Used Car Dealers Association of Malawi, lati nkofunika kuti boma liunikenso misonkho yomwe bungwe la MRA likumalipiritsa ponena kuti misonkhoyi ndi yokwera kwambiri.

Ganizoli ladza kutsatira mavuto omwe anthu ochita malondawa akukumana nawo mdziko muno ponena kuti akulephera kugulitsa malonda awo kamba koti nawo akumayenera kukweza mitengo ya katundu wawo zomwe zikupangitsa ogula kuti aziopa mitengoyi.

A Teputepu yemwe ndi mlembi wabungweli ndi omwe apereka pempholi pamene boma likukonzekera zokambirana zokhudza ndondomeko ya zachuma  ya chaka chino cha 2024 komanso 2025.

Iwo anati anthu ochuluka mdziko muno akulephera kuombola galimoto zawo pa chipata cholowera m’dziko muno cha Songwe zomwe zapangitsa kuti pazikhala magalimoto ochuluka osaomboledwa kamba ka misonkhoyi.

Bungweli kudzelanso mwa mlembi wamkuluyi lapemphaso Banki yayikulu mdziko ya Reserve Bank of Malawi kuti izichita machawi ndikuthandiza ndi ndalama zakunja pomwe zikufunika ndi cholinga choti ntchitoyi ipite pa tsogolo

Advertisement