…Khoti labwenzeretsa Mayi Chizuma
Tsiku lofa nyani mtengo ulionse umatelera. Boma la a Lazarus Chakwera lakumana nazo ku bwalo pamene oweruza ayimitsa kaye chiganizo choti awapumitse pa ntchito.
Bungwe la maloya mu dziko lino, Malawi Law Society, latenga chiletso pa chiganizo chofuna kuimitsa ntchito Mayi Martha Chizuma.
Malinga ndi zikalata za ku bwalo lamilandu lalikulu, bungweli lamang’ala ku bwalo kuti kuyimitsidwa ntchito kwa a Chizuma kunali kotsatsata ndondomeko.
Pounikirapo pa nkhaniyi, a bwalo ati akufunika kuti aunguze bwino lingaliro la boma loyimitsa ntchito a Chizuma. Koma podikira kuunguzaku, iwo ati Mayi Chizuma akuyenera azipitiriza ntchito yawo.
Malinga ndi zikalata zimene a Malawi24 taona, a bwalo ati Kalata imene mdzakazi wa a Chakwera, a Colleen Zamba, adalemba yoimika Mayi Chizuma pa ntchito sikuyenela kugwiritsidwa ntchito pa nthawi imene iwo akuchita kauniuni pa dandaulo lochoka ku bungwe la Malawi Law Society.
Mayi Chizuma anaimitsidwa ntchito atatenga zikalata zofuna kunjata mkulu wakale olondoloza milandu ya boma, kapena kuti DPP, a Steve Kayuni. Zinamvekanso kuti Mayi Chizuma amafuna kumanga Mayi Zamba koma izi bungwe la ACB linatsutsa.
Malipoti ati a Chakwera anauzidwa ndi owazungulira kuti Mayi Chizuma akufuna awamangire akazi wawo ndipo ndi pamene iwo adalamula kuti awayimitse kaye pa ntchito.
A Malawi odana ndi katangale aonetsa chisangalaro chawo ndi kubwenzeredwa pa udindo kwa Mayi Chizuma.
Follow us on Twitter: