Lero kuno, mawa uko, mkuja kwinako. Kunga galimoto za thasipoti zosamutsa anthu pamapeto a mwezi. Makhalidwe amenewa ndiwo akwiyitsa a malawi ena amene adndaula kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achulutsa u namayenda.
Pothilila ndemanga pa uthenga oti lero pa 2 December mtsogoleriyu akhala pa BICC pa mwambo wa kuthokoza, a Malawi ena anadabwa ndi kusakhazikika kwa a Chakwera. Dzulo pa 1 December, a Chakwera ankhala nawo pa mwambo okumbukila matenda a Edzi.
Dzana lomweli, a Chakwera anali mu mzinda wa Blantyre kumene anakadzodza nawo atsogoleri a mpingo wa Salvation Army. Mu masiku anayi okha, a Chakwera aonekela kugulu katatu mu Malawi muno. Kupatula maulendo a mu dziko momwe muno, iwonso ayendela mayiko a kunja oyandikana ndi Malawi.
Pothililapo ndemanga pa uthenga oti a Chakwera akhalanso bize lero ndi mwambo wina mu Lilongwe, a Malawi ochuluka anamudzudzula Chakwera ndi khalidwe lake longa ngati anadya matako a galu.
“Kumene muti mutenge nsabwe sikudziwika,” anadandaula choncho munthu wina pa tsamba la nyumba ya boma yomwe inalengeza nkhaniyi.
“Mukukathokoza chani kodi ku mwambo umenewu?” winanso anafunsa. “A Malawi akuvutika uku, konzani kaye mavuto awo.”
“Kodi nanga lachinayi, lachisanu kufika lamulungu ayendela kuti? A Malawi akuonatu kuti inu simukusintha zinthu ayi. Inu kanthawi komweka ma ulendo kuchuluka kuposa APM, chitukuko mupanga nthawi yanji ndiye? Apa tinangosintha boma osati kachitidwe ka zinthu,” winanso anadandaula motelo.
A Malawi ena afanizila u kamwendomnjira wa a Chakwera ndi wa Mayi Joyce Banda amene analamulilako kwa zaka ziwiri koma ulamulilo wawo unadzetsa mavuto a zaoneni kwa a Malawi.
“Zija ankapanga JB ndi izi, nanji pano ali ndi Tony Blair,” anatelo m’Malawi wina.
Maulendo a mtsogoleri wa dziko lino uyu achuluka tsopano ngakhale kuti anthu ogwila ntchito mu boma akudandaula za malipilo awo komanso za feteleza otchipa sizikulongosoka kwenikweni.