M’tsogoleri wa dziko lino wachotsa mkulu wa Bank yayikulu m’dziko lino ya Reserve bank a Wilson Banda kamba kolephera ntchito.
Malingana ndi anthu ena ogwira ntchito ku Capital Hill omwe atitsina khutu, panatsala miyezi 6 kuti kontarakiti ya a Banda ithe koma Chakwera wakanika kupilira ndipo wawona kuti ndi chanzeru kumuchotsa mkuluyu.
Mu ulamuliro wa a Banda ngati wamkulu wa Bank ya Reserve Bank dziko la Malawi lakhala likukumana ndi mavuto ambiri maka pa nkhani ya za chuma pomwe zinthu zakhala zikukwera mwezi uliwonse komanso kusowa kwa ndalama ya kunja.
Ngati wamkulu wa Bank’yi, Banda anagwetsa kwacha koyamba ndi 25 pelesenti mu 2022 kenako ndi 44 pelesenti mu chaka cha 2023. Inflation inakwela kuchoka pa 8.6 pelesenti mu chaka cha 2020 kufika
Pa 32.5 pelesenti mu chaka cha 2024.
Malipoti omwe atipeza dzina lina la yemwe asankhidwe ngati wamkulu wa Bank yi lapita kale kwa m’tsogoleri wa dziko lino. Pakadali pano, ofesi ya m’tsogoleri wa dziko lino ndi nduna sinalakhure kalikonse pa nkhaniyi.