Zipatala zambiri mulibe mankhwala – Phungu wadandaula

Advertisement
Jolobala

Phungu wa dera la kummawa kwa boma la Machinga a Esther Jolobala wadandaula kamba ka vuto lakusowa kwa mankhwala mzipatala lomwe lakula kwambiri m’dziko muno.

Phunguyi anadandaula za izi dzulo ku nyumba ya malamulo.

Jolobala anati zomvetsa chisoni kwambiri kuti zipatala zambiri zikukanika kupereka thandizo loyenera kwa anthu chifukwa cha kusowa kwa mankhwala.

“A malawi tikudziwa bwino lomwe kuti tikapita ku ma health centres athu ngakhale ku ma district hospital, anthu akumalemberedwa kuti akagule mankhwala ku ma pharmacies, ndipo izi ndi zomvetsa chisoni.

“A Malawi ndi mboni yanga kuzipatala kulibe mankhwala ndipo dzana dzanali tinatenga a chipatala kukayendera anthu olumala ku dera langa, koma kukanika ndithu kuti athe kuwapatsa pain killer ena omwe anali ndi ululu nde lero aziti mu zipatala muli mankhwala? Ndi zinthu zomvetsa chisoni kwambiri,” iwo anatero.

Koma poyankhapo, nduna ya za Umoyo a Kandodo Chiponda anati sizoona kuti mzipatala za dziko lino mulibemo mankhwala.

A Chiponda anawuzaso nyumba ya Malamulo kuti muzipatala za m’dziko muno muli mankhwala ochuluka ndi ma peresenti 70.

Iwo anati awuza akuluakulu a za umoyo m’maboma osiyanasiyana kuti apereke lipoti lokhudza kachulukidwe ka mankhwala amene ali nawo.

Advertisement