Sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Catherine Gotani Hara wapereka masiku asanu ndi awiri kwa Phungu wa Blantyre City South East a Sameer Suleman, kuti afotokoze chifukwa chomwe anapitila ku nkhokwe za feteleza za SFFRFM opanda kudziwitsa akuluakulu a ofesiyo.
A Suleman anapita ku SFFRFM komwe amafuna akawone ngatidi kuli feteleza, ndipo kupita kwawo Ku ofesiyi kunapangitsa a Malawi kudziwa kuti bungweli lilibe feteleza.
Ulendo wa a Suleman unakwiyitsa a phungu a Boma komanso akuluakulu ena chifukwa zinadziwika kuti boma la a Lazarus Chakwera lilibe feteleza omwe alimi ochepekedwa amagula motsika mtengo.
A Suleman anapita ku maloku ndi atolankhani.
Koma poyankha kalatayi, a Suleman akuti sakuona kuti panali kufunika kochita kudziwitsa SFFRFM zakupita kwawo ku malowo, chifukwa bungwelo ndi la Amalawi ndipo limayenera kutumikira Amalawiwo.
A Suleman atinso, akanawadziwitsa akuluakulu a ku SFFRFM kuti akupita ku ofesizo, sakanakapeza chilungamo koma chifukwa anapita modzidzimutsa anakapeza zoona zokhazokha zomwe ndikuphatikizapo kusapezeka kwa ogwira ntchito ena akuluakulu ku ofesizo pa nthawi ya ntchito.
Zomwe anapanga a Suleman kupita Ku SFFRM, naye wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Micheal Usi wakhala akupanga pomwe amapita muzipatala komanso ma office a Boma opanda kuwadziwitsa.