Bullets yagonjetsa Wanderers

Advertisement
TNM Super League

Zatha pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre, oyimbira ndiye waweluza kuti FCB Nyasa Big Bullets ndiyo mfumu ya Blantyre pakadali pano kutsatira  chipambano chomwe apeza pa adani awo a Mighty Mukuru  Wanderers mu chikho cha TNM Super League 2024.

Mphunzitsi wa Wanderers Meke Mwase wati kugonja kwa lero kwabwezeretsa m’mbuyo  timu yawo ndipo anyamata ake  sanayambe masewelo m’mene anawalangizira

 Iye anati anyamata ake  anatayilirana mu masewerawa  ndipo ati izi zawabwezeletsa m’mbuyo pang’ono,

Mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets  Calisto Pasuwa  wati iwo akhala akutaya ma points m’mbuyomu koma nthawi yakwana kuti ayesetse kumapeza chipambano m’masewero ambiri. 

Pasuwa wati ka chibwana kamene anyamata ake anapanga kumapeto kugoletsetsa chigoli pamene adani awo anali ndi anyamata ochepa m’bwalo chikanakhala chilango kwa iwo mu nthawi iliyonse.

Zigoli za Bullets zachoka kwa Ronald Chitiyo pa mphindi ya chi 6 ndi Babatunde Adepoju pa mphindi ya chi 40 ndipo chigoli chopukutira misonzi kuchoka kwa Thierry Tanjong Samar pamene Gomegzani Chirwa anachita zinjenje kumbuyo kuti masewerawa athere 1-2 kukomera Bullets.

Mnyamata wa Bullets Chrispin Mapemba ndiyee wakhala osewera wapamwamba mwa onse.

Zatelemu FCB Nyasa Big Bullets yatolera ndipo ili ndi ma points 40 mmasewero 23 pamene anyamata a ku Lali Lubani ali ndi ma points 44 m’masewero ofanana.

Mawa anyamata a Silver Strikers omwe akutsogolera pa  mndandanda wa chaka chino, akusungira ma points 50 ndipo akhale akukumana ndi Civil Service United mawa lamulungu mu mzinda wa Lilongwe.

Advertisement