Mtalimanja atule pansi udindo – Zipani zotsutsa

Advertisement
MEC

Zipani zotsutsa boma m’dziko muno zati mayi Annabel Mtalimanja atule pansi udindo wawo ngati mkulu wa Malawi Electoral Commission (MEC) kaamba koti alephera kugwira bwino ntchito.

Zipanizi zidanena izi pa msokhano wa atolankhani omwe zipani monga Alliance For Democracy (AFORD), United Transformation Movement (UTM), Democratic Progressive Party (DPP) anachititsa ku Lilongwe.

Zipanizi zinati ndizokaikitsa ngati MEC igwire bwino ntchito zake kamba koti akuluakulu ena ku MEC ndiotsatira chipani cholamula cha Malawi Congress.

Zipanizi zatinso chipani cholamula cha Malawi Congress chikufuna kudzabera ma voti chifukwa cha ganizo lake lobweretsa kampani ya Smartmatic kuti ibweretse zida zoyendetsera zisankho munjira ya makina kamba koti mbili ya kampaniyi siyabwino pa nkhani zoyendetsa zisankho.

A Timothy Mtambo omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha AFORD anati ndi odabwa kuti boma likukana ma auditors kuti adzakhalepo pa chisankho cha chaka cha mawa.

Nawo a Patricia Kaliati omwe ndi Mlembi wa Mkulu wa chipani cha UTM apempha bungwe la National Registration Bureau (NRB) kuti lichotse tsankho pa nkhani ya kalembera kamba koti mtsogoleri wa dziko lino adanena kale kuti iye siwatsankho.

Zipanizi zati ngati boma silichitapo kanthu pa zomwe zanena izo zichita zionetsero.

Advertisement