Bwalo la milandu la Zomba lamasula Mayi Jenita Matiasi yemwe adagamulidwa kuti akakhale kundende zaka zisanu pa mlandu wakupha khanda losabadwa la miyezi isanu ndi itatu (8).
Malingana ndi Legal Aid Bureau, Mayi Matiasi ndi nzika ya dziko la Mozambique ndipo adamangidwa chaka chino m’mwezi wa February koma anachita apilu mothandizidwa ndi Legal Aid Bureau pa mlanduwu womwe ndiwosemphana ndi gawo 231 lamalamulo adziko lino (Penal Code).
Assistant Director Zaheed Ndeketa mothandizana ndi Assistant Legal Aid Officers, Mirriam Kaunda ndi Tiyamike Kamtukule anaimilira mayi Matias.
“Pa nthawi yomwe ankapatsidwa chilango pa 3 March 2024, bwalo la Senior Resident Magistrate lidaunika kuti mayiyu adavomela kuti anachotsadi pathupi koma amayenera kutero masiku oyambilira osati pomwe pathupi panafika miyezi isanu ndi itatu.
“Pochita apilu, Assistant Director Zaheed Ndeketa anauza bwalo kuti mfundo zomwe anapereka ambali ya boma sizinali zokwanila kuti mayiyu amangidwe komanso kupatsidwa chilango,” yatero Legal Aid Bureau.
Nkhaniyi ikutinso bwalo laling’ono lomwe linapereka chilangolo lidalakwitsa kamba koti umboni woti mayiyu adachitadi izi sunali wokwanira.
Potero, mogwirizana ndi Legal Aid Bureau, bwaloli lati lachotsa chilango chomwe bwalo laling’ono linapereka kwa mayi Matiasi ndipo lamasula mayiyu pa mlanduwo.