Kodi oyimba akwathu kuno adzasiya liti kuyimbira a Malawi okha okha akapita mayiko akunja?

Advertisement
Mankhamba

“Pena vuto ndilakuti oyimba aku Malawi amakakamira kuyimba ngati akunja komweko ndiye anthu akunjawo zimangowamvekera ngati za kwawo komweko, ndi chifukwa zili zovuta kubooleza,” anatero Ben “Michael” Mankhamba.

Anaonjezeranso kuti vuto lalikulu lirinso ndi anthu omvera popeza kuti amakonda kumvera zakunja ndi chifukwa oyimba amafuna ayimbe zomwe omvera akukonda kuti azitha kupeza kanganyase.

“Komanso anthu omwe amayitana oyimba athu mayiko akunja saonetsa chidwi cholengezera ku mtundu onse m’dzikolo koma a Malawi okha basi,” Mankhamba anapenekera.

Pomwe Steve “Gwenda” Phombeya yemwe amakhala ku South Africa ndipo wakhala akuyitanitsa oyimba osiyanasiyana a kwathu kuno wati vuto liri ndi eni wake oyimba.

“Vuto ndilokuti oyimba aku Malawi sazigulitsa pa msika wakunja, ndipo ndizachilendo kuona munthu wa ku South Africa, Nigeria, Zimbabwe ndi mayiko ena akumvera nyimbo zaku Malawi.

Pomwe Mankhamba anayimabe pa mfundo yokuti vuto ndilatonse oyimba komanso omvera.

“Ndikukumbukira zaka za mbuyo dziko la Democratic Republic of Congo (DRC) linaletsa nyumba zowulutisira mawu kusewera nyimbo za mayiko ena zimene zinakakamiza anthu m’dzikomo kumangomvera nyimbo za kwawo pa chifukwa chimene zamba zakumeneko monga Kwasakwasa zinapeza msika wakunja,”iye anatero.

Katswiri wa nyimbo ya ” Kamba anga mwala-yu” anatinso kwathu kuno boma maka aphungu akunyumba ya malamulo atakhazikitsa lamulo longa anachitira anzathu ku DRC nyimbo komanso oyimba athu akhoza kudziwika pa msika wa mayiko akunja.

Anafotokozanso kuti pali band ina ku Malawi kuno yotchedwa “Madalitso” imapita ku mayiko aku ulaya pafupipafupi ndipo anthu omwe amayikonda ndi azungu chifukwa amagwiritsa luso lachikhalidwe chaku Malawi.

Ma lipoti pa tsamba la pa utatavo akusonyeza kuti Madalitso band ili ndi ma show 52 mu chaka chino ku mayiko monga Germany, United Kingdom, Switzerland, France ndi Italy kuchokera July mpaka October.

Izi zili chomwecho, Mankhamba yemwe anadziwika mu zaka zama 90’s ndi nyimbo monga “Gule wolobodoka” “Chinangwa” ndi zina zambiri akuti posachedwapa akutulutsa nyimbo yatsopano

Advertisement