Mayi Bomba anjatidwa ataba galimoto ziwiri zobweleka

Advertisement

Mayi wa zaka 42 ali m’manja mwa apolisi munzinda wa Lilongwe pomuganizira kuti anaba galimoto ziwiri zomwe anabwereka kenaka nkukazigwilitsa ntchito ngati chikole pokatenga ngongole ya K27 million.

Foster Benjamin yemwe ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi kum’mawa mchigawo chapakati wazindikira mayi wolimba ntimayu ngati a Towera Bomba omwe amangidwa Lachiwiri kunyumba kwawo ku Area 12 ku Lilongwe.

Bomba
Anjatidwa

Apolisi ati miyezi yapitayi Bomba adabweleka galimotozi kuchokera kwa anthu awiri osiya koma wakhala asakuoneka komaso anasiya kuyankha foni akayimbilidwa kuti akabweze galimotozi zomwe zinachititsa eni katunduyu kukadandaula ku polisi.

Potsatira kafukufuku, Bomba wamangidwa ndipo zadziwika kuti mayiyu anakasintha umwini wa galimoto zonsezi mkuziyika mu dzina lawo la Towera Diana Bomba.

Atatelo, Bomba adagwiritsa ntchito galimoto imodzi kukatenga ngongole ya K15 million kwa munthu wina ku Area 49 ku Lilongwe ndi galimoto in a yo kukatenga ngongole ya K12 million kwa mayi wina wochita malonda ku Mzuzu.

Bomba yemwe ndiwochokera m’boma la Dedza, akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe milandu itatu; wina wakuba galimoto, kupanga zikalata zachinyengo komanso kuchita ukathyali.

Advertisement