Komiti imene imawunikira anthu omwe ali oyenera kukapikisana nawo m’maudindo osiyanasiyana ku msonkhano waukulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) yati idalandira zikalata kuchokera kwa anthu 224 omwe adasonyeza chidwi pofuna kupikisana pa mipando yosiyanasiyana ku msonkhano waukulu wa chipanichi.
Ngakhale izi zili chonchi, komitiyi yapeza kuti pa anthu 224 wa, 204 ndi amene ali ovomelezeka kupikisana nawo pa zisankhozi.
Izi zadziwika lero kum’mawaku pamene chipanichi chimachititsa msonkhano wa atolankhani ku likulu la chipanichi munzinda wa Lilongwe pofuna kudziwitsa mtundu wa aMalawi komanso otsatira chipanichi mmene zokonzekera msonkhano waukulu wa chipanichi ukuyendera.
Chipanichi chikuyembekezeka kuchititsa msonkhano wake waukulu kuyambira pa 8 mpaka pa 10 August ku Bingu International Convention Centre (BICC) mu nzinda wa Lilongwe.
Wapampando wa msonkhanowu a Kezzie Msukwa wati komiti yomwe imawunikila za anthu okapikisana nawo ku monkhanowu mwa zina inawunikira mbiri ya anthuwa komanso kuti akhale okhazikika mchipanichi.
Chipanichi m’mbuyomu chidalengezapo kuti munthu kuti adzapikisane nawo pa udindo mchipanichi, akuyenera kukhala kuti wakhala membala wa chipanichi kwa zaka zosachepera ziwiri.
Poyankhula pa msonkhanowu, ofalitsa nkhani m’chipanichi a Ezekiel Ching’oma adati a Lazarus Chakwera alibe opikisana nawo ku msonkhanowu ngakhale kuti chipanichi chidapeleka mwayi woti anthu athe kutero.
Maina omwe avomelezedwa kukapikisana nawo pa chisankhochi ali motere:
Mtsogoleri wa MCP
1.Lazarus Chakwera
Wachiriri woyamba wa mtsogoleri wa MCP
1.Catherine Gotani Hara
2.Kezzie Msukwa
3.Moses Kumkuyu
4.Ahmed Dassu
5.Kenneth Zikhale Ng’oma
Wachiriri kwa wachiwiri wa mtsogoleri wa MCP
1.Abida Mia
2.Anussa Hassan
Mlembi wamkulu wa chipani
1.Chris Chaima Banda
2.Richard Chimwendo Banda
3.Simplex Chithyola Banda
4.Dyson Kamphambe
5.Albert Mbawala
6.Eisenhower Nduwa Mkaka
Msungichuma wa chipani
1.Rhino Chiphiko
2.Jacob Hara
3.Yusuf Matumula
4.John Paul
Ndipo pofuna kuwonetsetsa kuti chisankhochi chachitika mwa chilungamo, a Ching’oma ati nthumwi zochokera m’mipingo yosiyanasiyana ndizo zavomelezedwa kuti zizayendetse mwambo wa chisankhochi.
Ngakhale chipanichi chalengeza za anthu amene avomelezedwa kukapikisana nawo ku msonkhanowu, bwalo la milandu likuyembekezeka kupeleka chigamulo chake pa dandaulo lomwe anthu ena m’chipanichi adakamang’ala ku bwalo la milandu pa lamulo loletsa mamembala omwe sadathe zaka ziwiri ali ma membala a chipanichi kutenga nawo gawo pa mpikisanowu.
M’modzi mwa akuluakulu amene asiyidwa pa mndandanda wa opikisana nawo ndi a Vitumbiko Mumba.