Kasitomala zikamuvuta timakambirana – FINCA 

Advertisement
FINCA

Kampani ya FINCA yomwe ikusangalala kuti yatha zaka makumi atatu (30) ikugwira ntchito za za chuma m’dziko muno, yati ndi bodza lankunkhuniza kuti imalanda makasitomala ake katundu zikawavuta pobweza ngongole.

Izi ndi malingana ndi mkulu wa kampaniyi a Charles Bello omwe anena izi Lolemba pa 5 August 2024 pakutha pamwambo wosangalalira zaka 30 zomwe kampaniyi yakhala ili m’dziko muno omwe unachitikira kulikulu lakampaniyi munzinda wa Blantyre.

FINCA
Bello: tili ndi mgwirizano wabwino ndi makasitomala athu.

A Bello anati FINCA yakwanitsa kukhala m’dziko muno zaka zonsezi kamba ka mgwirizano wabwino ndi makasitomala ake, ndipo iwo athetsa manong’onong’o omwe akhala ikuveka kuti kampaniyi imagwiritsa ntchito ziphona kukalanda katundu wa kasitomala yemwe akukanika kubweza ngongole.

Iwo ati; “Makasitomala athu timamvana nawo, ngati pali mavuto timawalimbikitsa kuti abwere adzanene kuti ine zandivuta tipange bwanji. Ntchito ya FINCA ndikubweleketsa ndalama osati kulanda anthu katundu. Anthu ena amanena kuti FINCA imalanda zinthu, ayi sitilanda katundu.

“Makasitomala athu akavutika, zinthu sizikuyenda timawalimbikitsa kuti abwere tikambirane tiwone kuti njirayi tiyenda bwanji. Timathandizana nawo ndipo mu nthawi yomwe zinthu zili bwino amatha kubweza ngongole yawo.”

A Bello alonjeza kuti kampani ya FINCA ipitilirabe kutumikira anthu m’dziko muno mwaukadaulo pankhani za zachuma kuphatikiza kupitilirabe kubwereketsa anthu ndalama pachiongora dzanja chosaboola mthumba.

A Phyllis Kalichero ochokera ku Chilobwe mu nzinda wa Blantyre anachitira umboni kuti apindura zedi ndi ntchito za zachuma zomwe kampani ya FINCA yakhala ikupeleka pa zaka 30 zimenezi.

Iwo ati; “Ngongole zomwe ndakhala ndikutenga ku kampani ya FINCA zandipindulira kwambiri pa banja langa. Poyamba ndinalibe kuthekera koti nditha kumalipilira ana anga sukulu, koma pano zikutheka. Ndinakwanitsa kugula ziweto komaso ndimapanga bizinezi, zonsezi ndi kamba ka kampani ya FINCA.”

Mwambo wachisangalowu unayamba ndi ulendo wandawala motsogozedwa ndi bandi ya a polisi kuchokera pa khothi m’Blantyre kukafika pa Besto Bello, kanaka kubweleraso mu Blantyre ku ofesi za kampaniyi komwe kunali malonje, kuvina komaso kudya nkhomaliro.

Advertisement