Zina ukamva kamba anga mwala: Mwana wa nzika yothawa kwawo yemwenso sanakwane zaka 18, ali pandandanda okanyongedwa m’dziko la Somaliland kamba kopha m’modzi mwa anthu omwe ankafuna kumupanga chiwembu.
Pa 11 February chaka chino, bwalo la milandu m’dziko la Somaliland linagamula Abshir Saleban Hussein wosakwana zaka 18, yemwe bambo ake anathawa m’dziko la Ethiopia kuti akanyongedwe kamba kakupha Nimcan Mohamed Omar.
Maumboni akukhothi akusonyeza kuti Hussein anapha Omar podziteteza pa nthawi yomwe iye anachitidwa chiwembu ndi anthu angapo omwe akuti ankafuna kuchotsa moyo wake.
Malamulo a dziko la Somaliland samalora kuti mwana wosakwana zaka 18 anyongedwe, koma zikuveka kuti khothili linamupatsa Hussein chigamulochi kamba koti malemu Omar anali wochokera mtundu wa Isaaq omwe akuti ndi komwe kumachokera mtsogoleri wa dzikolo Muse Bihi Abdi komaso akuluakulu ena aboma.
Loya wa Hussein, Hamdi Mahmoud anakamang’ala za nkhaniyi ku bwalo lalikulu m’dzikolo kuti lisinthe chilangocho koma zakanika kamba ka ubale omwe unalipo pa malemu Omar ndi akuluakulu ena maboma kuphatikizapo mkulu wa mabwalo a milandu a Adam Haji Aji Ahmed.
Pakadali pano bungwe la Cornell Center on the Death Penalty Worldwide layambitsa kampeni yoti dziko la Somaliland lichotse Hussein pa ndandanda wa anthu oti anyongedwe.
Bungweli likulimbikitsa anthu komaso mabungwe ena kuti alembele kalata mkulu wa ma bwalo a milanduyu Aji Ahmed kuti chilangochi chisinthidwe.
Chomvetsa chisoni nchakuti Hussein ndi mwana yemwe amathandiza banja lakwawo pankhani ya zofunika zonse za pakhomo kuphatikizapo zakudya kamba koti bambo ake akudwala matenda amuubongo.