Bambo anyongedwa chifukwa chopezeka ndi mankhwala ozunguza ubongo mdziko la Singapore

Advertisement

Wolemba: Gracious Zinazi

Bambo wa zaka 34 wanyongedwa lero lachitatu m’dziko la Singapore chifukwa chopezeka ndi mankhwala ozunguza ubongo a heroin okwana ma sipuni atatu mu chaka cha 2009.

Bamboyu ndi Nagaenthran Dharmalingam, yemwe kwawo kwenikweni ndi ku Malaysia. Mayi ake komanso omuimirira pa mulandu anayesetsa kuti amupulumutse potenga ziletso komanso kufotokoza kuti ma lipoti akuchipatala akuonetsa kuti iye ali ndi vuto la mu ubongo, koma izi sizinatheke.

Dziko la Singapore ndi limodzi mwa maiko omwe zilango zake zili zokhwima kwa anthu opezeka ndi mankhwala ozunguza ubongo ndipo Dhamalingam wakhala akuyembekezera chilango chonyongedwa chifukwa cha mlanduwu kwa zaka khumi kuchokera pomwe anamupeza ndi mankhwalawa kumbali ina ya ntchafu yake yakumanzere.

Panthawi yomva mulanduwu iye wakhala akunena kuti anakakamizidwa komanso kuopsezedwa kuti atengere mankhwala oletsedwawa m’dzikomo, kenako anavomera kuti anachita izi chifukwa chofuna ndalama. Mu chaka cha 2015 anayesera kupempha kuti amusinthire chilango chonyongachi ndipo mmalo mwake akakhale ku ndende moyo wake onse chifukwa ali ndi mthenda yamu ubongo, naye omuimirira pa mulandu anatsimikiza izi ponena kuti kunyonga munthu otere ndikupsanya malamulo aufulu wa anthu pa dziko lonse lapansi, koma khothi linapitirira ndi chigamulo chomunyonga ndipo linati iye alibe nthendayi chifukwa amatha kupanga chisankho pakati pa chabwino ndi choipa. Nalo pempho lopita kwa mtsogoleri wa dziko la Singapore Halimah Yacob kuti amukhululukire linakanidwa chaka chatha.

Dzulo khothi lakananso chiletso chomwe mai ake a Nagaenthran anatenga choletsa kumunyonga, ndipo wanyongedwa lero lachitatu pa April 27, 2022. Mchimwene wake Navin Kumar, wa zaka 22, watsimikiza izi ndipo wati akuyembekezera thupi lake lifike mdziko la Malaysia kuti akachite mwambo wa maliro mu mzinda wa Ipoh.

Anthu pafupipafupi mazana atatu anayatsa makendulo ndikuchita mdikiro mzinda wa Singapore lolemba posagwirizana ndi chigamulochi. Enanso anachita mdikiro monga uwu ku Singapore High Commission mdera la Kuala Lumpar lachiwiri usiku kupempha kuti mzibamboyu amumvere chisoni.

Nawo anthu ochuluka mmasamba amchezo kuchoka mmaiko osiyanasiyana aonetsa nkwiyo komanso chisoni ndizomwe zachitikazi, kuphatikizapo khumutcha waku Britain Richard Branson komanso katswiri opanga mafilimu Stephen Ferry.

Advertisement