Norman Chisale apezeka osalakwa pa milandu yoposera isanu

Advertisement
Norman Chisale

Bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe lagamula kuti Norman Chisale ndi mfulu pa milandu isanu ndi umodzi (6) kuphatikiza omwe anamangidwa kamba konena mau onyazitsa nduna ya za chilungamo a Titus Mvalo. 

A Chisale omwe anali mkulu owona za chitetezo cha mtsogoleri wa kale wa dziko lino Peter Mutharika, anamangidwa kangapo konse mbuyomu ndipo anatsekulilidwa milandu isanu ndi imodzi.

Lero Lachitatu, a Chisale anaonekera ku khothi kuti akamve tsogolo la milandu yonse yomwe amaganizilidwa komwe oweruza milandu a Roderick Michongwe wagamula kuti mkuluyu ndi mfulu pa milandu yonseyi. 

Pa mlandu omwe anamangidwa mu November chaka chatha potsatira kuulutsidwa kwa pologalamu ina pa kanema ya Zodiak momwe akuti ananyoza ndikuopseza a Mvalo powanena kuti “Chi Minister,” bwalo lapezeka kuti mbali ya boma yalephera pa zinthu zina.

Mwazina a Michongwe ati a Chisale ndi mfulu pa mlandu onyoza ogwira ntchito m’boma kamba koti mbali ya boma yalephera kuonetsa kuti kunena kuti “Chi Minister” ndi mlandu woti munthu atha kukakhala nawo ku ndende.

Pa mlandu omwe a Chisale amaganizilidwa kuti adaopseza a Mvalo, a Michongwe ati a mbali ya boma alepheranso kusonyeza kuti a Chisale adaopseza kufika pa mlingo woti anakatha kupweteka munthu.

Kuonjezera apo, Chisale ndi mfulu pa mlandu ofuna kusokoneza milandu yawo ina yomwe ili kubwalo la milandu.

Advertisement