Mzika za dziko la Zambia zapulumutsa khanda lomwe linakwirilidwa mphepete mwa tsinje

Advertisement
Zambian Police

Anthu okhala m’dera la Sinazongwe mu dziko la Zambia apulumutsa mwana wina obadwa kumene amene anakwirilidwa mu mphepete mwa tsinje pamene amaganizira kuti ndi njoka ndipo anali ndi maganizo oti aiphe.

Malinga ndi nyumba youlutsa mau ya Byta FM dzikolo yati Cabel Sianyangu wa zaka 28 zakubadwa ndi amene anaona pamalopo pakutukula ndipo anali ndi maganizo oti ndi njoka.

Pa nthawiyi anali atapatuka mu mseu kuti ayankhe foni pamene anali pa ulendo wake  ndipo  ataona izi sanachedwe koma kumemeza anthu ena ozungulira  m’deralo ndipo anafika pamalopo  ndi zida zoti akukapha njoka.

Atafukula pa dzenjelo  anapeza kuti ndi mwana wobadwa kumene amene anakwirilidwa ali wa moyo .

Wachiwiri wa mkulu  wa polisi m’dera la kumwera kwa dzikolo, Moono Namalongo ndiye watsikimiza za nkhaniyi ndipo wati izi zinachitika pa 11 July, 2024 ndipo mwanayu akusungidwa ku chipatala cha boma koma  a polisi ali mkati mofufuza mwini khandalo. 

Advertisement