Bambo wamangidwa poponyera ana ake awiri m’chitsime

Advertisement
Malawi24

Bambo wa zaka 32 yemwe anayambana ndi mkazi wake, ali m’manja mwa apolisi mu nzinda wa Lilongwe pomuganizira kuti amafuna kupha ana ake awiri powaponyera muchitsime cha madzi momwe akhalamo masiku atatu.

Wofalitsa nkhani pa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu, wazindikira bamboyo ngati Aubrey Madzinkusamba yemwe amafuna kupha mwana wake wa mkazi wa zaka zisanu ndi zitatu komaso wina wa mamuna wa zaka zinayi.

A Chigalu ati pa 4 July chaka chino, bambo Madzinkusamba omwe amakhala m’mudzi mwa Matapa m’boma la Lilongwe, anasemphana chichewa ndi mkazi wawo pa nkhani zina za m’banja, ndipo awiriwa anagwirizana kuti banja lawo lithe.

Apolisi ati Loweluka lapitali pa 6 July, bambo oganizilidwayu anatenga ana awo awiriwa ndi kukawaponya m’chitsime china ku dera la Likuni m’boma lomweli la Lilongwe ati kamba koti samafuna kuti nkaziyo atenge anawo azikakhara nawo.

Mkaziyo atadabwa kuti kwa ka nthawi anawo sakuwoneka, anamufusa mamuna wake wakaleyo yemwe adanama kuti wakawasungitsa anawo ku malo ena.

Mayiyo posakhutitsidwa ndi yankholo anakanena ku polisi ya Chinsapo omwe sanachedwe koma kuthira dzingwe mkuluyu.

Atawapanikiza ndi mafunso, bambo Madzinkusamba anawalondolera a polisiwo ku Likuni komwe anawa anawaponya muchitsime chakuya pafupifupi ma mita makumi atatu momweso munali madzi.

Mwamwayi anawa anawapeza a moyo kamba koti muchitsimemo munali madzi ochepa zomwe zinachititsa kuti azikwanitsa kupuma kamba koti m’masiku onsewo mitu ya anawo imaonekera siyinamire.

Apolisi mothandizana ndi anthu ena ozungulira deralo anapulumutsa anawo omwe pakadalipano agonekedwa pa chipatala cha Kamuzu Central komwe akulandira thandizo la mankhwala.

Bambo Madzinkusamba omwe ndi wochokera m’mudzi wa Kasiya mfumu yaikulu Khongoni ku Lilongwe konko, akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wofuna kupha.

Advertisement