Ku Malawi kwabadwa chipani china Cha PDP

Advertisement

Mtsongoleri wazipani zotsutsa boma kunyumba yamalamulo yemwenso ndi phungu wanyumba yamalamulo wa dera lapakati m’boma la Mulanje Kondwani Nankhumwa walengeza kuti wayambitsa chipani chake cha People’s Development Party (PDP).

A Nankhumwa, womwe anachotsedwa mu chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) alengeza izi patsamba lawo la mchenzo la Facebook.

Nankhumwa wanena kuti apangitsa msonkhano wa atolankhani posachedwapa komwe akafotokoze zambiri zokhudza chipani chomwe chipangitse msonkhano wake wawukulu chaka chino.

Iwo ati chipanichi chalembetsedwa kale mu mkawundula wazipani mdziko muno.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.