Ofesi yamaphunziro ku Machinga yabweza ganizo lokweza ndalama ya welofeya

Advertisement

Potsatira zionetsero zomwe aphunzitsi msukulu za pulayimale m’boma la Machinga anapanga Lachinayi, ofesi ya maphunziro m’bomali yabweza ganizo lake lokweza ndalama ya welofeya yomwe inachoka pa K1000 ndikufika pa K3000.

M’mawa wa Lachinayi, aphunzitsi a msukulu za pulayimale m’bomali anasiya kaye choko komaso ma “Lesson plan” ndikuthamangira ku ofesi ya mkulu wa maphunziro m’bomalo posagwirizana ndikukwezedwa kwa ndalama ya welofeya yomwe mphunzitsi aliyese amadulidwa pakutha pa mwezi uliwonse.

Aphunzitsiwa ati anali odabwa kuti pa malipiro a mwezi wa April, mphunzitsi aliyese m’bomalo wadulidwa ndalama zokwana K3000 m’malo mwa K1000 yomwe amayenera akudulidwa ngati ya welofeya.

Aphunzitsiwa anadandaula kuti sanauzidwe za kukwezedwa kwa ndalamayi ndipo akuti aka sikoyamba izi kuchitika kamba koti mbuyomu, ofesiyi inakwezaso ndalamayi kuchoka pa K500 kufika pa K1000 koma osawadziwitsa.

Apa aphunzitsiwa anaitanizana kuchokera m’masukulu a pulayimale monga St Teleza, Mtubwi, Liwonde LEA, Chinguni, Mkasaulo komaso Namalasa ndikulowera ku ofesi ya nkulu wa maphunziro m’bomali kwinaku nyimbo za milandu zili pakamwa.

Atafika kumeneku, aphunzitsiwa anakumana ndi mkulu wa maphunziro m’bomali a Douglas Namikungulu yemwe anamutulira nkhawa zawo zonse kuphatikaza nkhani yakukwezedwa kwa ndalama ya welofeyayi.

Poyankhapo pa madandaulo aphunzitsiwa, a Namikungulu alamura kuti ganizo lokweza ndalama ya welofeyayi, libwezedwe kaye kufikira mtsogolomu pomwe ma gulu onse okhudzidwa akumane m’nkachipinda komatu.

A Namikungulu alamura kuti podziwa kuti ndikovuta kubweza ndalamayi, mphunzitsi aliyese m’bomali asadulidweso ndalama ya welofeya ya mwezi wa May komaso June.

Mkulu wa maphunziroyu wapelekaso mwayi kwa aphunzitsi m’bomali kuti akambirane usanafike mwezi wa July za zomwe akufuna zizichitika pa ndondomeko yowadula ndalama ya welofeyayi, ndipo izi akuti zikupeleka danga kwa aphunzitsiwa kusankha kuti ndondomekoyi ipitilire kapena ithe.

Kuwonjezera apo, a Namikungulu alamuraso kuti komiti imene imayendetsa za welofeya, kutsogoloku iyitanitse nkumano wa mbali zonse zokhudzidwa kuti akakambirane zoyenera kuchita.

M’modzi mwa aphunzitsi okhudzidwa yemwe tayankhula naye koma anapempha kuti tisamutchule dzina lake, wati aphunzitsi onse m’bomali agwirizana ndi mfundozi.

“Mkumano wathu ndi a CEO, wayenda bwino ndipo tasangalatsidwa ndi zigamulo zomwe apeleka pa nkhawa zomwe tinawatulira,” watelo m’modzi m aphunzitsi okhudzidwa. 

Advertisement