Aphunzitsi akuchita zionetsero ku Machinga

Advertisement

Aphunzitsi m’boma la Machinga athamangira ku ofesi ya mkulu wa maphunziro m’bomalo komwe akuti akufuna kupeza mayankho pa ganizo la ofesiyo yokweza ndalama ya welofeya   opanda chidziwitso. 

Malingana ndi m’modzi mwa aphunzitsi, yemwe tayankhula naye, yemwe afuna kuti tisawatchule dzina, akuti ofesi ya za maphunziro m’bomali yadula ndalamayi pa malipilo a mwezi wa April, 2024. 

Mphunzitsiyu watiuza kuti poyamba mphunzitsi aliyese amadulidwa ndalama ya welofeya yokwana K500 pa mwezi koma inakwezedwa ndikufika pa K1000 opanda ofesiyo kufotokoza zifukwa zake. 

Lachitatu lapitali ogwira ntchito m’boma alandira ndalama za malipiro a mwezi wa April koma aphuzitsiwa ati anali odabwa kuti ofesiyi yawadula ma K3000 zomwe zawapangitsa kuti athamangire ku ofesi ya mkulu wa maphunziroyu kuti akawafotokozere tchutchu pa kudulidwa  ndalamaku. 

“Ifeyo tadabwa kuti ofesiyi yakweza ndalama ya welfare ifeyo osatiuza, nde tikufuna atifotokezere bwino bwino. Poyambaso ofesiyi inapanga zimenezizi, inakweza kuchoka pa K500 kufika pa 1000 koma ife osatiuza. 

“Apa ofesiyi yapangaso chimodzimodziso, nde tikuona kuti sizoona zimenezi, amayenera atiuze kaye kuti akweza ndalamayo asanatidule. Nde tabwera kuno kuti atiyankhule za nkhaniyi,” watelo mphunzitsiyo. 

Ena mwa aphunzitsi omwe akupanga nawo zionetserozi achokera sukulu ngati; St Teleza, Mtubwi, Liwonde LEA, Chinguni, Mkasaulo komaso Namalasa, kungotchulapo ochepa chabe. 

Pakadali pano ofesi ya maphunziro m’bomali siyinayankhule ndipo ife tipitilira kukupatsirani zambiri za nkhaniyi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.