Alimi alangizidwa kuti apewe kugulitsa zokolora kwa ma Venda

Advertisement

Mabungwe a Rays of Hope, Save the Children ndi YODEP, alangiza alimi m’dziko muno kuti apewe kugulitsa zokolora zawo kwa ma Venda pa mitengo yosavomerezeka.

Izi zayankhulidwa pomwe ma bungwewa akuchita chionetsero cha zaulimi mudzi wa Chikombole m’dera la Nsipe, mfumu yaikulu Kwataine m’boma la Ntcheu.

Iwo alangizanso alimiwa kuti asunge chakudya chokwanira komanso kugulitsa mbewu zawo pa mitengo yovomerezeka imene boma lalengeza posachedwapa pofuna kupewa vuto la njala m’tsogolomu.

M’modzi mwa alingizi a za ulimi ndi umoyo wa anthu ku Future 4 All Malawi, Mark Phiri wapempha alimi kuti awonetsetse kuti mbewu zawo zauma bwino komanso kuti asunga chakudya chokwanira kuti ana atetezedwe ku chiopsezo cha njala.

M’mawu ake, m’modzi mwa alimi, Fanny Monjeza, a m’mudzi mwa Kamtema mfumu ya ikulu Kwataine, ati kusowa kwa chakudya pa banja kumadzetsa nkhanza kwa ana komaso kuwakakamiza kuti akwatire mwa nsanga.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.