Amangidwa kamba ka kupha mzake mchaka cha 2015

Advertisement

Mawu oti mulandu si uwola aphelezera pomwe Apolisi ku Bolero m’boma la Rumphi amanga Giuele Mfune pomuganizira kuti adapha Magowa Mtambo mchaka cha 2015.

A Mfune akhala akuthawa kuyambira 2015 ndipo amangidwa anthu akufuna kwabwino atatsina khutu apolisi zakupezeka kwa a Mfune ku Bolero .

Malinga ndi m’neneri wa polisi ku Rumphi Sub Inspector Noel Kamchenga pa November 8, 2015, malemuyo anali akumwa mowa ndi anzake komwe Mfune anabwera n’kumumenya kawiri pamphumi komanso kumutu ndi nkhuni.

Magowa anavulazidwa kwambiri mutu ndipo anakagonekedwa ku chipatala cha Bolero Rural komwe adatulutsidwa pa November 16, 2015 atalandira chithandizo.

Pa 8 December 2015, adawatengeraso kuchipatala cha chikulu cha Rumphi komwe adamwalira pa 10 December akulandira chithandizo.

Azachipatala atayeza thupi la malemuwo adapeza kuti imfa idachitika chifukwa cha kuwonongeka kwa mitsempha yamagazi kuchokera kumutu kupita kumsana.

A Mfune akaonekera kubwalo la milandu kukayankha mlandu wakupha.

A Mfune amachokera m’mudzi wa Tengamapu mfumu yayikulu Chikulamayembe, m’boma la Rumphi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.