Agwidwa ndi bomba pomwe amafuna kukalithira nsika

Advertisement

Anyamata awiri akusungidwa mchitokosi cha apolisi ku Mwanza atagwidwa ndi bomba pa malo ochitira chipikisheni munsewu wa Mwanza-Blantyre pomwe iwo anali pa ulendo wawo okalithira nsika bombali.

A Hope Kasakula yemwe ndi wofalitsa nkhani pa polisi ya mwanza wati anyamata awiriwa ndi a Andrew Gauti Stephano azaka 31 ndi a Justin Lewis azaka 30.

Kasakula wati awiriwa anabisa bombali musaka, ndipo anayamba kuliyatsa liwiro la mtondo wadooka ataona kuti apolisi akuchita chipikisheni.

Izi zinachititsa jenkha apolisiwo mpaka anayamba kuwathamangitsa ndikuwagwira.

Atagwidwa, apolisiwo anapeza kuti abambo awiriwa ananyamula bomba lomwe iwo amafuna kukaligulitsa pa mtengo wa 1.2 miliyoni kwacha mu mzinda wa Blantyre.

Apa abambo awiliwa anauzanso apolisiwa kuti yemwe amakamugulitsayo amachotsamo timadzi mu bombalo tomwe tili tofunikira angakhale kuti sadaulule ntchito yake.

Advertisement