Boma lakweza ngongole yomwe ophunzira sukulu za Ukachenjede amalandira

Advertisement
Simplex Chithyola Banda

Nduna yoona za chuma mdziko muno a Simplex Chithyola Banda walengeza za kukwera kwa ngongole yomwe ophunzira a msukulu za ukachenjede amalandira kuchoka pa K350, 000 pachaka kufika pa K560,000.

A Chithyola Banda anena izi lero masana m’nyumba ya malamulo poyankhapo kutsatira madando omwe zipani zotsutsa boma komanso makomiti ena adapereka m’nyumbayi pankhani yofuna kukweza ndalamazi.

Izi zadza pomwe phungu wina wa nyumba ya malamulo mchigawo chapakati ku Zomba a McNice Abu Naliwa, atapempha boma kuti likonze ndondomeko ya ngongole za ophunzira kuti ikhale yothandiza komanso yopezeka kwa ophunzira omwe akusowa thandizo.

Sabata lapitalo mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus Chakwera adauza nduna ya zamaphunziro kuti achite mkumano ndi bungwe loona zamaphunziro la National Council for Higher Education kuti aunikire za ngongole yomwe ophunzira a msukulu za ukachenjede amalandira.

Ndalamazi ndizo zimathandizira ophunzira msukuluzi kugula zinthu zowayenereza kuphatikizapo makope ndi zina.

Advertisement