…Ena adandaula kuti bizinesi yawo yophika kachasu yaima
Anthu ochuluka adasonkhana mu shopu ya Chipiku Plus mu mzinda wa Zomba kukanganirana kugula shuga ndipo anthu amakhala maola atatu kapena anayi ali pa mzere asadagule.
Malawi24 idayankhula ndi Mai Bridget Vinti omwe adali nawo panzere wogula shugayo ndipo anadandaula kuti akulu akulu a Chipiku Plus akuwalola kugula paketi imodzi ya shuga ndipo adati koma ngati munthu angagule zinthu zopitilira 3,000 Kwacha akumulola kugula mapaketi awiri.
Mai Vinti adati adakhala pamzere kwa maola opitilira anayi (4) kuti agule paketi imodzi ndipo adati izi ndi zodandaulitsa ku dziko la Malawi.
Iwo ati amafuna kugula mapaketi awiri kuti mwina akathe kugwiritsa ntchito kwamasiku angapo koma adawuzidwa kuti agule paketi imodzi yokha ngati sagula zinthu zina zowonjedzera zosachepera 3,000 Kwacha.
Mai Vinti adatinso kusowa kwa shuga kwapangitsa kuti anthu ena azivutika popeza amaphika mowa wa kachasu ndipo amapeza ndalama zothandidzira mabanja awo monga kulipilira ana awo sukulu komanso kugula zakudya m’makomo mwao koma izi akulephera popeza bizinesi yomwe amachita yophika mowa yaima.
“Tipemphe Boma kuti lichite zothekera kuti shuga ayambe kupezeka popeza tikumavutika ndipo ena ochita malonda apedzelapo mwayi akumatigulitsa shuga mtengo wa 4000 paketi imodzi,” adatero Mai Bridget Vinti.
Ndipo a Isaac Vetuwa omwe amakhala kwa Namalaka adati akhala panzere kwama ola atatu kudikilira kuti agule shuga.
A Vetuwa adati anthu akudandaula chifukwa shuga sakadayenera kumasowa popedlza akupangidwa M’malawi momuno ndipo adati lero alephera kupita kuntchito chifukwa chodikilira kugula shuga modzi.
Anthu ena omwe sadafune kuti tiwatchule mayina awo adandaula kuti shuga wabwera wambiri mu Chipiku Plus ku Zomba koma anthu ena abizinesi akumabwera kumadzagula kuti adzikagulitsa pamtengo wokwera.