Koma a Tonse ndiye ndi zidebe zenizeni, Chakwera alongeze azipita – DPP yatsukuluza Tonse

Advertisement

Chipani chotsutsa cha DPP chasambwadza akuluakulu a Kongeresi ndi UTM kuti ndi osadziwa kanthu. A chipanichi ati utsogoleri wa Tonse ndi osapatsa chikoka ndipo atsogoleri ake ndi zidebe chabe zopanda kanthu koma phokoso basi.

Malinga ndi chikalata chimene chipanichi chatulutsa potsatira kafukufuku wa Afrobarometer amene waonetsa kuti a Malawi ochuluka akufinyika kamba ka utsogoleri wa Tonse, chipani cha DPP chati izi si zodabwitsa kwenikweni chifukwa atsogoleri a Tonse’wa amaonetsa kuti alibe ukadaulo.

Chikalatachi chomwe chasayiniridwa ndi mneneri wa DPP a Shadric Namalomba chati iwo akugwirizana kwathunthu ndi zopeza za kafukufukuyi ndipo ati choyenera kuchita ndi choti a Chakwera alongeze azipita basi.

Mwa zina a katswiri a kafukufuku anapeza kuti pa a Malawi khumi ali onse, mmodzi yekha ndiye akupeza mpumulo mu chuma cha a Chakwera. A chipani cha DPP ati izi ndi zoona ndipo iwo awalitsapo kunena kuti miyandamiyanda ya a Malawi ikuzunzika.

Chipanichi chatinso kamba ka mavuto a zachuma obwela ndi utsogoleri wa a Chakwera, mu dziko muno tsopano mulibe chitetezo ndipo a Malawi ochuluka akuzikhweza.

Malinga ndi chipani cha DPP, ati yankho ku zonsezi ndi loti a Chakwera atule pansi udindo chifukwa a Malawi ochuluka akuoneka kuti sakukondwa ndi utsogoleri wawo.

DPP yalonjezanso kuti iyo ndiyo ili ndi kuthekera kokonza zinthu ku Malawi.

Advertisement