Musadele nkhawa, tikonza vuto la Magetsi

Advertisement

Kampani yogulitsa magetsi m’dziko muno ya ESCOM yatsimikizira anthu okhala ku Majiga 2 ntauni ya Balaka kuti akhala atakonza vuto lomwe la magetsi pofika lolemba, pa 25 March, 2024.

Izi zili mchikalata chomwe mkulu wa kampaniyi mu ma boma a Mangochi, Machinga, Ntcheu komanso Balaka, a Martin Mbwandira asainila pamodzi ndi m’modzi wa otsogolera nzikazi a Pretorius Halidi.

Kum’mawaku, nzika zokhudzidwazi zinakhamukila ku ofesi ya kampaniyi ku Balaka komwe zidayamba kuchita m’bindikiro.

Atsogoleri a nzika zokhudzidwawa analowa mu kachipinda komata komwe amakambirana ndi akuluakulu a kampaniyi pa zatsogolo ya nkhaniyi.

Komabe, nzikazi zatemetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti sizisiya m’bindikiro wawo mpaka vutoli litathetsedwa.

Advertisement