Chakwera lero akuyendera Tropha Estate, Kwithu Kitchen

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Pomwe akupitilira kuyendera zinthu zosiyanasiyana mchigawo cha ku mpoto, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, lero ali m’boma la Mzimba komwe akuyendera Tropha Estate ndipo akatelo apita ku Mzuzu kukayendera malo ophikira zinthu zosiyanasiyana a Kwithu Kitchen.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa yofotokoza zomwe mtsogoleri wa dzikoyu achite lero pomwe akupitilira kuyendera madera osiyanasiyana mchigawo cha ku mpoto ndipo kalatayi wasayinira ndi mlembi wa mkulu wa boma, mayi Colleen Zamba.

Malingana ndi chi kalatachi, a Chakwera akuyembekezeka kukafika ku Tropha Estate yomwe ili mdera la Ekwendeni m’boma la Mzimba m’mawa lero komwe akaone momwe ntchito za ulimi zikuchitikira pa esiteti imeneyi yomwe mwa zina pa malimidwa mtedza wa macadamia.

Akachoka ku esiteti imeneyi, nzika yoyamba ya dziko linoyi ithamangira mu mzinda wa Mzuzu komwe ikakhale ndi zochitika zingapo kuphatikiza kuyendera malo omwe azimayi amaphika zinthu zosiyanasiyana omwe amatchedwa Kwithu Kitchen.

Pomalizira, a Chakwera masana a lero, akuyembekezeka kukumana ndi ochita malonda omwe si a boma ku Mzuzu komweko, komwe mwa zina akufuna kukawalimbikitsa.

Sabata yonseyi, a Chakwera akhala ali mchigawo cha kumpoto kuyendera zinthu zosiyanasiyana.

Advertisement