Fostina Mbemba wapambana mpikisano wa Mzuzu Half Marathon

Advertisement

Fostina Mbemba ndi amene wathamanga kuposa atsikana anzake mu mpikisano wa Mzuzu City Half Marathon lero.

Mtsikanayu analibutsa liwiro ngati kulibe mawa ndipo iye anathamanga mtunda okwana 21 kilomitazi pa ola limodzi ndi mphindi zokwana makumi awili ndi zisanu.

Wachiwiri kupambana ndi Teleza Master ndipo iye anathamanga makilomita okwana 21 mu ola limodzi ndi mphindi zokwana makumi awili ndi zisanu ndi imodzi.

Ndipo wachitatu kupambana ndi Nalise Chirwa amene wathamanga mtunda omwewu pa ola limodzi ndi mphindi zokwana makumi awili ndi zisanu ndi zinayi.

Inde inu m’mene zililimu woyamba wapita ndi 1.5 miliyoni, wotsatira wake 1 miliyoni pamene wachitatu 500,000 kwacha.

Advertisement