Chikondi Mwanyali ndi amene wapambana masewera a Mzuzu City Half Marathon atathamanga mtunda otalika makilomita okwana 21 pa ola imodzi ndi mphindi zokwana zisanu ndi chimodzi.
Mkulu wina amenenso wakonkhomola lekodi ndi Chancy Master pamene wakhala pa nambala yachiwiri atathamanga mtunda otalika makilomita okwana 21 pa ola limodzi ndi mphindi zokwana zisanu ndi ziwili.
Chikondi Mwanyali amene wakhala pa nambala yoyamba apita ndi ndalama zokwana 1.5 miliyoni kwacha pamene Chancy Master apita ndi ndalama zokwana 1 miliyoni kwacha.
Inde inu anyamata amenewa amachita mokhala ngati akuuluka kuli kulikumba liwiro la ntondo wadooka.