Atsikana osakwana zaka 18 oposa 9800 anabereka ana ku Blantyre mu 2023

Advertisement

Akatswiri pa nkhani za umoyo ati kuchepa kwa kapezedwe ka njira za kulera komaso kusiyila sukulu pa njira ndi zina zimene zikuonjezera chiwerengero cha atsikana omwe akubereka asanafike zaka 18.

Mkulu wa za umoyo ndi achinyamata khonsolo ya Blantyre, Gift Kawalazila wati pafupipafupi atsikana 48 pa atsikana 100 aliwonse amene ali osapyola zaka 15 zakubadwa amakhala pa chiopsezo chobereka nsanga chifukwa chosowa maphunziro akagwiritsidwe ntchito ka njira za kulera komaso zikhulupiriro za zikhalidwe ndi zipembedzo ndi zina mwa zimene zikukolezera vutoli.

“Boma la Blantyre lili ndi atsikana ochuluka oti ndiosapyola zaka 18 zakubadwa koma anabelekako kale chifukwa  chosowa maphunziro okwanira pa kwagwiritsidwe ntchito ka njira za kulera,” anatero a Kawalazira poyankhula ndi Malawi News Agency.

Mukuonjezera kwawo, anati mu chaka cha 2022, pafupipafupi atsikana okwana 9,519  anabereka ana koma ali  osapopsyola zaka 18 zakubadwa pamene mu chaka cha 2023 analipo  pafupipafupi 9,809 zimene zili zotsatira za nkhani ya zikhulupiriro za makolo komanso kusowekera kwa maphunziro apaderadera pa nkhani ya kulera kwa kuchipatala.

Mu mau ake, mkulu wa Bungwe la Family Planning Association of Malawi (FPAM), Donald Makwawa, wati kuchepa kwa zipatala zing’onozing’ono mma’dera akumidzi komanso kusowekera kwa mauthenga okhudza nkhani za kulera ndi zina mwa zimene zikukolezera vutoli.

“Tikugwira ntchito ndi unduna wa za moyo poonetsetsa kuti anthu akulandira uthenga ndi maphunziro  oyenera okhudza nkhani za kulera ndi cholinga chofuna kuchepetsa vutoli,” a Makwawa anauza Malawi News Agency.

Iwo anaonjezeraso kunena kuti pafunikira kufikira akuluakulu a zachipembedzo ndi cholinga choti azilimbikitsa anthu awo kutenga ndi kugwiritsa ntchito njira za kulera.

M’modzi mwa atsikana amene ali osakwana zaka 18 amene amakhala m’dera la Mbayani anati anatenga pakati ali ndi zaka 14 mu chaka cha 2023 ali STD 5 ku sukulu ina ku Chilomoni.

“Mai anga sanadziwe kuti ndili ndi pakati chifukwa nthawi zambiri amakhala ali ku ntchito. Kwa miyezi itatu ndinkapitabe ku sukulu ngakhale ndinali ndi pakati kufikira pamene aneba anauza Mai anga kuti ndili ndi pakati,” iwo anatero.

Mtsikanayu ali ndi mwana wa miyezi 9 ndipo anaonjezera kunena kuti anakumana ndi vutoli chofukwa chokakamizika ndi anzake amene amayenda nawo.

Advertisement