Unduna wati pali chiopsezo cha madzi osefukira ku mpoto

Advertisement
Malawi Tropical Cyclone

Unduna Woona za Madzi ndi Ukhondo wati kuyambira pa 7 mpaka pa 14 mwezi uno, madera ambiri kumpoto kwa dziko lino komanso m’mbali mwa nyanja, akhalabe akulandira mvula yamphamvu, zomwe zikupeleka chiopsezo choti kumaderawa kutha kukhala madzi osefukira.

Izi ndi malinga chikalatachi chomwe unduna watulutsa chomwe wasainira ndi m’modzi mwa akuluakulu ake a James Chitete ndipo chati ina mwa mitsinje yomwe itha kusefukira chifukwa cha mvulayi ndi North Rukuru, South Rukuru, Hara, Nyungwe, Wovwe, Songwe, Kyungu, Lufila, Limphasa, Nkhula, Lipimbi, Dwambazi, Dwangwa, Bua, Luweya, Linthipe, Chirua, Lingadzi, Kaombe, Lifidzi komanso Nadzipuru.

Kutsatira chiopsezochi, nthambi yowona za madzi ku undunawu, ikulangiza anthu kuti apewe kukhazikika ndi kuwoloka mitsinje yomwe ili ndi madzi ochuluka komanso kukhala tcheru akamayenda m’madera omwe atchulidwa kuti ali pa chiopsezowa.

Kupatula apo, madera omwe ali m’mphepete mwa mitsinje yomwe yatchulidwayi akulangizidwanso kuti adzitsatira njira yochenjeza anthu za kusefukira kwa madzi (Community Based Flood Warning Systems (CBFEWS)) pofuna kupewa kutaya miyoyo chifukwa cha kusefukira kwa madziku.

Anthu akulangizidwanso kuti adzitsatira mwa chidwi mauthenga omwe undunawu ukumatulutsa nthawi ndi nthawi pa zomwe zikuchitika zokhudza kuchuluka kwa madzi.

Advertisement