Mphunzitsi ali mchitokosi kamba kogwililira mwana

Advertisement

Apolisi m’boma la Rumphi akusunga mchitokosi wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya Mzungutwa a Wonderson Shaba a zaka 34 zakubadwa powaganizira kuti anagwililira mtsikana wa zaka 14.

Mneneri wa apolisi m’boma la Rumphi, Noel Kamchenga ndiye watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti bambo Shaba anapalamula mlanduwu kuchokera mwezi wa November, 2023 mpaka February, 2024.

“Mayi ake a mwanayi ndi amene anazadziwitsa apolisi atazindikira kuti mtsikanayu akumagonana ndi munthu wina,” anatero a Shaba.

Mayi wa mwanayi anapitiriza kunena kuti oganiziridwawu amapatsa ndalama mwanayi ndipo amamulonjeza kuti adzamulipira sukulu fizi ku sekondale.

Zotsatira za chipatala cha Mzokoto zikusonyeza kuti mwanayu amagonana ndi munthu.

Advertisement