Chakwera akatsekulira chipatala cha khansa

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, lero akhala akutsekulira chipatala cha nthenda ya khansa mu nzinda wa Blantyre chomwe wamanga ndi mpondamatiki Thom Mpinganjira.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa Lolemba yomwe wasainira ndi Colleen Zamba yemwe ndi mlembi wamkulu mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna zake (OPC).

Malingana ndi kalatayi, a Chakwera akuyenera kukatsekulira chipatalachi masana a lero Lachiwiri pa 5 March, 2024 ndipo mwambo wake ukuyembekezeka kuyamba nthawi ya 1 koloko.

Mpondamatiki Thom Mpinganjira pamodzi ndi anthu ena awiri akunja, ndi omwe amanga chipatala chothandiza anthu odwala matenda a khansa-chi ndipo chipatalachi chidzitchedwa Blantyre International Cancer Center.

M’mbuyomu, a Mpinganjira anauzaso atolankhani kuti malingaliro omanga chipatalachi anabwera powona kuvutika komwe anthu odwala khansa amakumana nako pofuna akupeza thandizo la mankhwala omwe amayenera kutumizidwa kunja kwa dziko lino.

Kupatula apo khumutchayu, anati chifukwa china chachikulu chomangira chipatalachi ndi kamba kokhudzidwa ndi imfa ya nkazi wawo oyamba, Barbara, yemwe anamwalira Lachisanu pa 04 January, 2019 atadwala nthenda ya khansa.

Mwezi wa December chaka chatha, akuluakulu ena a chipatalachi, anauza atolankhani nkhani kuti chipatalachi chomwe chamangidwa mphepete mwa nsewu wa Magalasi ndipo ndichoyamba mdziko muno, chikhala cholipilitsa koma nthawi imeneyo anafotokoza kuti kukambirana ndi akuluakulu a boma kunali kuli mkati kuti mitengo yake ikhale yotsikirako kuti anthu ambiri adzikwanitsa.

Advertisement