Immigration yati kubwezeretsa sisitimu kukutheka

Advertisement

Nthambi yowona za anthu olowa ndi otuluka m’dziko muno ya DICS, yati ntchito yobwezeretsa sisitimu yake yomwe inasokonezedwa ndi akathyali ena ikubala zipatso ndipo akuti pali chiyembekezo chokwanilitsa ntchitoyi asanathe masiku 21 omwe anapeleka mtsogoleri wa dziko lino.

Izi zikubwera pomwe kuyambira January chaka chino, nthambiyi siyikukwanitsa kugwira ntchito zake zina kuphatikiza kusindikiza ziphaso zoyendera kamba koti akuti anthu ena amtopola anasokoneza sisitimu yomwe nthambiyi imagwiritsa ntchito.

Potsatira izi, mwezi watha mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera analamura kuti akuluakulu a nthambi ya DICS awonetsetse kuti chilichonse chabwelera nchimake ku nthambiyi pasanathe masiku makumi awiri ndi mphambu imodzi (21).

Pofika Lolemba pa 4 March lomwe linali tsiku la khumi ndi mphambu ziwiri (12) kuchokera pomwe a Chakwera analamura, nthambiyi yati ntchito yobwezeretsa sisitimu yake ikuyenda bwino kwambiri ndipo itha posachedwapa.

Kudzera mu kalata yomwe nthambiyi yatulutsa, pali chiyembekezo choti ntchito yobwezeretsa sisitimu yakeyi itha kufika kumapeto masiku 21 omwe Chakwera anapeleka ku nthambiyi asanafike.

“Patsiku lakhumi ndi chiwiri kuchokera pomwe mtsogoleri wa dziko la Malawi Dr. Lazarus McCarthy Chakwera analamula kuti nthambi yowona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno iyambenso ntchito yopereka ziphaso zoyendera yomwe idasokonekera posachedwapa chifukwa cha kuphwanya malamulo a pa cybersecurity, nthambiyi ikufuna kudziwitsa anthu onse kuti ntchitoyi ikubala zipatso.

“Ndi gulu la akadaulo lomwe likugwira ntchito mosalekeza ndi Amalawi okhudzidwa, nthambiyi ili ndi chikhulupiliro kuti cholinga choyambiranso ntchito yosindikiza ziphaso zoyendera pasanathe masiku 21 omwe mtsogoleri wa dziko lino adakhazikitsa, kukwaniritsa,” yatelo mbali ina ya kalatayi.

Nthambiyi yati pakadali pano ntchitoyi ikugwirika ndi akatswiri ochokera ku nthambi zosiyanasiyana za boma ndi maunduna komanso kuphatikizaposo akatswiri pa nkhani za makina intaneti ochokera ku bungwe la MACRA komaso bungwe la ICT Association of Malawi (ICTAM).

Nthambiyi yatsindika kuti yabwezeretsa ma lipoti onse omwe anasowa a anthu omwe ali kale ndi ziphaso zoyendera ndipo yalimbikitsa kuti omwe ali ndi ziphasozi azisamale ponena kuti kusokonekera kwa sisitimuku, sikukhudza kagwiritsidwe ntchito ka mapasipoti omwe adaperekedwa kale ndi nthambiyi.

Advertisement