Red Cross yati ipitiriza kufikira anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi

Advertisement

Bungwe la Malawi Red Cross Society lati lidzipereka kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi mu chigawo chapakati ndi kumpoto kwa dziko lino chifukwa ndipo lati chiwerengero cha anthu omwe akusowekera thandizo ndi malo okhala ndi chochuluka.

Mkulu oyang’anira zochitikita ndi chitukuko cha anthu mu bungweli, Prisca Chisale, ndiye anayankhula izi pamene amagawa zipangizo za ku khitchini, mikeka, ma tenti, sopo komaso zipangizo zina zambiri kwa anthu omwe akhudzidwa ndi vuto la kusefukira kwa madzi omwe akukhala pa Lungu pulayimale sukulu pansi pa mfumu yaikulu Mphonde m’boma la Nkhotakota.

“Tikuyetsetsa kutolera thandizo losiyanasiyana kuti tifikire anthuwa,” anatero mukuyankhula kwawo a Chisale.

Amene anaimila bwanamkubwa wa m’bomalo, Sirilo Magomero, wati pali masomphenya omanga malo oyembekezela kuti anthuwa adzikakhala chifukwa pakanali pano ambiri ali ma sukulu.

Kusefukira kwa madzi kwakhudza anthu pafupipafupi 11,000 ndipo anthu 6,000 alibe pokhala pamene anthu 4 ndi amene atsikira kuli chete m’bomalo.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement