Nthambi ya Immigration yatsutsa kuti maina a anthu omwe ali ndi ziphaso zoyendera asowa

Advertisement

Nthambi yoona zolowa ndi kutuluka mdziko muno ya DICS yati mphekesera zomwe zimkuveka kuti nthambiyi ilibe dzina ngakhale limodzi la anthu omwe ali ndi ziphaso zoyendera mdziko muno, ndizabodza.

Nkhaniyi ikubwera pomwe nthambi ya DICS kufikira pano ikukanikabe kusindikiza ziphaso zoyendera kapena kugwira ntchito iliyose kamba ka akathyali ena omwe akuti anasokoneza sisitimu ya nthambiyi m’mwezi wa January chaka chino.

Zikuveka kuti akathyaliwa, akulamura boma la Malawi kuti lipeleke ndalama zokwana K2 biliyoni kwacha kwa iwo ndicholinga choti nthambiyi iyambileso kugwiritsa ntchito sisitimu ya DICS yomwe inasokonezayo.

Potsatira nkhaniyi, nsabatayi munamveka manong’onong’o kuti makina omwe nthambi ya DICS imagwiritsa ntchito popangira ziphaso zoyendela, awonongeka kothelatu kotelo kuti kukhala kovuta kuwagwiritsaso ntchito kwa panopa.

Kupatula apo anthu ena amaonjezeraso kuti kamba ka kuonongeka kwambiri kwa makina opangira ziphasowa, nthambiyi ilibeso mndandanda wa maina a anthu omwe ali ndi ziphasozi zoyendera mdziko muno.

Koma kudzera mu kalata yomwe wasainila ndi ofalitsa nkhani za nthambiyi a Wellington Chiponde, nthambiyi yati manong’onong’o onse omwe akuvekawa ndi bodza la nkunkhuniza ndipo yati anthu asakhale ndi mantha kamba ka zomwe zikuvekazi.

Mu kalatayi a Chiponde  alimbikitsaso nzika za dziko lino kuti zikhale ndi chikhulupiliro choti makinawa a nthambiyi akonzedwa ndipo abwelera mchimake posachedwapa.

Advertisement