Chidakwa chakana ngongole ya thobwa: Techno Brain ikuti sizikuyikhudza za kusokonekera kwa ntchito yopanga mapasipoti

Advertisement

Fisi anakana nsatsi: kampani ya Techno Brain yomwe ikuganizilidwa kuti ndi yomwe yasokoneza sisitimu ya nthambi yosindikiza ziphaso zoyendera mdziko muno yati iyo siyikukhudzidwa ndikusokonezedwa kwa sisitimuyi koma yati boma silikuyankhula kanthu paupangili omwe kampaniyi inapeleka pofuna kuthetsa vutoli.

Nkhaniyi yayamba mwezi wa January pomwe manong’onong’ono akhala akumveka kuti nthambi ya “Immigration and Citizenship Services (DICS)” ikulephera kusindikiza ziphaso zoyendera kamba koti anthu ena awupandu asokoneza njira za chinsinsi (system) zomwe nthambiyi imagwiritsa ntchito pogwira ntchito yake.

Podziwa kuti mvula ikagwa kuchuluka zoliralira, anthu ena akhala akuloza chala kampani ya Techno Brain kuti ndi yomwe yapanga chipongwechi kamba koti zikuveka kuti nthambi ya DICS imafuna kusindikiza ziphaso mwachinyengo.

Koma poyankhapo za kulozedwa chala kwawo pa nkhaniyi, kampani ya Techno Brain kudzera mu kalata yomwe yatulutsa Lachiwiri pa 27 February, 2024, yakanitsitsa kuti siyikudziwapo kanthu za kusokonezedwa kwa “system” ya nthambi yosindikiza ziphaso mdziko muno.

Kampaniyi yati iyo siingapange dziko lino chipongwe cha mtundu otelewu ndipo yawulura kuti nkhaniyi itadziwika kumene, iyo inatsina khutu boma la Malawi kudzera ku nthambi ya DICS pa zomwe ikuyenera kuchita kuti “system” iyambileso kugwira ntchito koma akuti mpaka pano boma silinayankhe kanthu.

“Techno Brain ikutsutsa nkhani zomwe posachedwapa zalembedwa zotilumikiza molakwika ndi kuyimitsidwa kwa posachedwa kwa njira zosindikiza ziphaso zoyendera mdziko muno. Techno Brain siyimapanga mchitidwe wa “cyberattack” ndipo, m’malo mwake, tidayankha mwachangu pa pempho lomwe boma la Malawi linatipempha kuti tithandizire kuthetsa vutoli mu January, 2024.

“Tili ndi chisoni chachikulu kwa nzika za Malawi ndipo tidachita kauniuni wa momwe zinthu ziliri ndipo tinapereka ku boma la Malawi maganizo athu othandiza kuti vutoli lithe. Mpaka pano, sitinamveponso yankho kuchokera ku boma la Malawi pa mfundo zomwe tinawapatsa.

Techno Brain idasamutsa ndikupereka kwathunthu magwiridwe antchito ndi kayendetsedwe ka kusindikiza ziphaso ku Department of Immigration and Citizenship Services (DICS) mu June 2023.

Izi zidachitika motsatira chigamulo chomwe Techno Brain ndi boma la Malawi adachita kutsatira kuthetsedwa nsanga kwa mgwirizano wa Techno Brain pa ma ePassport mu October, 2022,” yatelo mbali ina ya kalata ya Techno Brain.

Kampaniyi yafotokozaso kuti chithereni mgwirizano wake ndi boma la Malawi mu 2022, chili chose chokhudza kusindikiza ziphaso zoyendera, zimapangidwa ndi nthambi ya “Immigration” ngakhale kuti kangapo konse nthambiyi inapempha kampaniyi kuti iyithandize pomwe zinasokonekeraso mbuyomu.

Kampaniyi inamaliza kalatayi ndikunena kuti ikukhulupirira kuti boma la Malawi litha kuthetsa vutoli mwachangu.

Advertisement