Boma lati layamba ntchito yogawa ufa ku maanja okhudzidwa ndi njala

Advertisement
Maize flour which Malawi Government with support from WFP is giving to Malawians

Boma kudzera ku Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DoDMA) tsopano layamba ntchito yogawa ufa ku maanja omwe akhudzidwa ndi njala m’dziko muno pansi pa ndondomeko ya Lean Season Response.

Malingana ndi DoDMA, ntchitoyi yakhazikitsidwa pa 24 February, 2024 ndipo ufa wu ndi wokwana matani 23,000.

M’mawu awo, nduna Yoona Zofalitsa Nkhani a Moses Kunkuyu pokhazikitsa ntchitoyi anati boma lionetsetsa kuti maanja omwe akuvutika ndi njala m’dziko muno athandizidwa ndipo palibe yemwe afe ndi njala.

Ndipo Mkulu wa World Food Programme (WFP) kuno ku Malawi a Paul Turnbull, anati bungwe lake liri ndi chidwi chopitiliza kuthandiza boma kufikira maanja okhudzidwa komanso kupereka chiyembekezo mu nyengo yosowa chakudya.

Boma lafikila maanja okwana 798,319 kuyambira m’mwezi wa October chaka chatha omwe ndi anthu pafupifupi 3,592,435. Maanjawa alandira thumba la chimanga m’maboma onse (28) komanso mizinda inayi ya m’dziko muno pomwe maanja 174,003 omwe ndi anthu pafupifupi 783,013 alandira ndalama zokwana K50,000.00 pa mwezi.

Ufa omwe uzigawidwawu, ukuperekedwa ndi thandizo la ndalama lochokera ku World Bank kudzera ku World Food Programme Malawi ndipo ufikira maanja 397,778 omwe ndi anthu pafupifupi 1,790,000.

Advertisement