Mlendo Uladi Mussa akapikisana nawo pa mipando  iwiri ku MCP

Advertisement
Uladi Mussa (R) during a times exclusive interview with Brian Banda

Yemwe anali m’modzi mwa akulu akulu ku chipani cha Democratic Progressive  DPP a Uladi Mussa ndipo pakali pano adalowa chipani  cha Malawi Congress (MCP) ati iwo atafatsa kuwelenga malamulo a chipanichi tsopano ali ndi mangongolomela okapikisana nawo pa mipando iwiri ku msonkhano waukulu omwe chipani cha MCP  chipangitse.

Poyankhula pa wailesi ya kanema wa Times ndi Brian Banda mu pulogalamu ya Times Exclusive, a Mussa ati iwo atawelenga malamulo a MCP akuona kuti malinga ndi luso lawo komanso nzeru zawo iwo akapikisana nawo pa mphando wa Wokopa anthu (Campaign Director) ngakhalenso pa mpando  wa wachiwiri kwa mtsogoleri kumene.

A Mussa womwe atuluka ku ndende posachedwapa  ati iwo ali ndi chikoka cha nkhani-nkhani kuti abweretse anthu kuchokera ku DPP popeza pano abweretsa kale ena ochuluka kubwera ku MCP.

“Ma udindo amewawa ndi amene ine ndikapikisane nawo ndipo ine ndiasapota a Chakwera mpaka 2030 wooh ndi imene ntchito imene agwire chenji golo imeneyo,” a Mussa anatero mkulongosola kwawo.

A Mussa MU mwezi wa Januwale analowa chipani cha  MCP pa sukulu ya Pulayimale ya Katelera m’boma la  Salima pamene  chipani chawo chomwe anali  Cha DPP chidawayimitsa kwa miyezi isanu ndi Inayi(9) chifukwa chophwanya  dongosolo  la chipanichi.

A Mussa  womwe anali mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo cha pakati akhala akuthandiza a Kondwani Nankhumwa ndipo awiriwa adawachotsela limodzi pamodzi ndi ena omwe amayenda kuthandizila a Nankhumwa kuti adzayimile utsogoleri wa chipanichi ukadzafika msonkhano wawuku.

Advertisement